2. Mlowam’malo wa dzina lakelake
• Mlowam’malo uyu amagwiritsidwa ntchito
m’malo mwa dzina la munthu ndipo alipo a
mitundu itatu motere:
• Mlowam’malo wakalozamwini
• Mlowam’malo wakalozamnzako
• Mlowam’malo wakalozawina
3. Mlowam’malo waumwini
• Uyu ndi mlowam’malo yemwe amadziwitsa za
mwini wake wa chinthu. Mlowam’maloyu
amadziwika ndi masinde monga awa; -ke, -wo,
-thu, -nga ndi -nu
4. Mlowam’malo wowerengera
• Uyu ndi mlowam’malo wonena za
chiwerengero chenicheni cha zinthu.
Mlowam’maloyu amadziwika ndi masinde
monga awa: -modzi, -wiri, -tatu, -nayi, -sanu